Zochitika pa Tsiku la Chikuku 07 June 2026 ku Parishi ya Maula

Pa 7th June ndi Tsiku la Chikuku, Patsikuli Misa zidzakhala monga mwa nthawi zonse kupatula Misa ya Chilatini yomwe siidzakhalapo. Misa ya Chilatini idzakhalapo pa 14th June 2026.

 

(Chithunzi: Ambuye George Tambala pamwambo wakupembedza Ambuye Yesu okhala mu Ukaristia ku Maula Cathedral)
(Chithunzi: Ambuye George Tambala pamwambo wakupembedza Ambuye Yesu okhala mu Ukaristia ku Maula Cathedral)

Misa yathu ya Chichewa idzakhalira ku Podium nthawi ya 10 koloko yomwe idzatsogozane ndi Mwambo woyenda ndi Chikuku. Ndipo tidzamalizira  ndi Udalitso.

Pachifukwa ichi Miphakati ikupemphedwa kudzabwera kuno ku Tchalictchi kudzakongoletsa Malo oyendamo ndi Ambuye Yesu Loweruka pa 06 June 2026, nthawi ya 8 koloko m’mawa.

Dongosolo la Malo lili motere:-

  1. St. Francis Mphakati, ku Podium
  2. St. Monica,  kuyambira Nsewu wopita ku podium kulekezera pakati pa mpanda  wa Abambo.
  3. St. Mary, Kuyambira pakati pa Mpanda wa Abambo mpaka pothera ka nsewu kafumbi popit ku Podium.
  4. St. Jude, Kuyambira ku gate yolowera mpaka kuyang’ana kufupi ndi gate ya kwa Bishop.
  5. St. Teleza kuchokera pa Hump kulekezera kufupi ndi ku ma toilet
  6. St. Peter. Carpark ground kuyang’ana ku Groto
  7. St. Paul kuchokera pa Hump ya ma Toilet mpaka kukhomo la kutchalitchi

Mdipiti kuchoka ku Podium kupita ku Tchalitchi udzayenda motere

Miphakati idzayenda ndi a choir akuyimba nyimbo za Ukaristia motere:-

  1. Choir one – St. Mary ndi St. Monica
  2. CMA Choir –St. Paul ndi St. Jude
  3. Choir Two- St. Peter ndi St. Teleza
  4. CWA Chair –St. Francis ndi Alendo onse
Share the Post:

Related Posts