2.1 Tikuthokoza a Mphakati wa St. Theresa chifukwa chotsogolera chipembedzo sabata yathayi ndi kukonza mtchalitchi muno komanso kupeleka mphatso zomwe zili kuguwa kuno. Kuyambira mawa omwe ayambe kuyendetsa chipembedzo ndi a MPHAKATI WA St. Francis ndipo Mulungu otsatira adzayendetse Chipembedzo ndi a MPHAKATI WA ST. Mary
2.2 Zikomo kwambiri anzathu a Choir ya Gregorio potsogolera nyimbo ndi chipembedzo pa nsembe ya Ukaristia ino, mwatithandiza kupemphera bwino patsiku lalero ndipo tikukupemphani kuti mupitilize. Kwaya yomwe idzatsogolere nyimbo LAMULUNGU LA YESU KHRISTU MFUMU ndi CHOIR ya St. Maria Cresencia
2.3 Tikudziwitsidwa kuti tayamba njira yatsopano yoperekera chopereka ku mchalitchi muno pogwiritsa ntchito Airtel Money, komanso Airtel App popanga Scan QR code .
2.4 Onse amene akufuna kubwerera Mmasacrament akupemphedwa kubweretsa makalata kuchokera ku Mphakati ndikudzalembetsa ku office ya Parish.
2.5 Mwezi wa November ndi Mwezi okumbukira Mizimu ya Mpurigatorio, Tiyeni tiyesetse Kumawapempherera
2.6 Pa 18th November 2026 ndi tsiku la Birthday ya Archbishop ndi Auxiliary Bishop athu Tiyeni tidzawafunire Mafuno abwino ndikuwapempherera
2.7 Pa 5 December tidzakhala ndi mbindikiro wa advent, kuno ku Parish, tiyeni tonse tidzafike.
