A Nuncio Atsogolera Nsembe ya Misa ya Chichewa ku Parishi ya Maula

Akhristu pa parishi ya Our Lady of Africa, Maula Cathedral mu Arkidayosizi ya Lilongwe, ayamikira kazembe wa a Papa m’maiko a Malawi ndi Zambia, Archbishop Gian Luca Perici, kaamba kotsogolera Nsembe ya Ukaristiya mchichewa pa 20 September 2026 lomwe ilinali La Mulungu la 25 pa chaka

Ambuye Perici anatsogolera Misa ya 10 koloko m’mawa, yomwe yakhala yapadera kwa akhristu.

Polankhula pambuyo pa mwambo wa Nsembe ya Misa, Bambo Mfumu a Parish ya Maula, bambo Francis Lekaleka, ati akhristu asangalala kwambiri kuona kazembe wa aPapa akutsogolera mwambowu mchilankhulo chawo.

Bambo Lekaleka kuwerenga mthenga
Bambo Lekaleka kuwerenga mthenga

Bambo Lekaleka ati nthawi zambiri a Nuncio amatsogolera Misa mchingerezi, choncho kuona akuyesetsa kutsogolera Misa yonse mchichewa chakhala chinthu chosangalatsa pakati pa akhristu.

“Chosangalatsa kwambiri chinali choti a Nuncio athu koyamba apemphere nafe Misa ya Chichewa. Si kawirikawiri kuona a Nuncio akutsogolera Misa ya Chichewa. Kwa ife chinali chinthu chosangalatsa kwambiri kuona Nuncio akutsogolera Misa yonse mchichewa,” atero Bambo Lekaleka.

Wapampando wa Parishiyi, a Dorica Chirwa, ati ulendo wa Archbishop Perici lero wakhala wosangalatsa kwambiri, makamaka chifukwa chotsogolera Misa yonse mchichewa.

Mai Chirwa kuthokoza a Nuncio pambuyo pansembe ya Misa
Mai Chirwa kuthokoza a Nuncio pambuyo pansembe ya Misa

“Chachikulu chimene chinatidabwitsa komanso kutikondweretsa kwambiri ndichakuti Misa inali ya Chichewa ndipo awerenga Chichewa Misa yonse. Tikuwathokoza kwambiri ndipo tipitiriza kuwapempherera,” atero a Chirwa.

A Chirwa apempha akhristu kuti apitirize kupempherera Archbishop Perici komanso aPapa, kuti Mulungu apitirize kuwadalitsa pamene akutumikira Mpingo wa Katolika.

Archbishop Perici anali mdziko muno pomwe anadzakhala nawo pa chikondwerero cha zaka 125 za mpingo wakatolika chiukhazikitsireni kuno ku Malawi.

Wolemba ndi Edwin Sitima

Wojambula zithunzi ndi Mathews Jerry Banda

Share the Post:

Related Posts