Akayidi andende ya Maula ku Lilongwe alimbikitsidwa kuti akhale odalira Mulungu pa moyo wawo watsiku ndi tsiku.
Bambo mthandizi a parishiyi, bambo Peter Makina ndi omwe alimbikitsa andendewa pamwambo wansembe ya Misa yomwe anatsogolera m’mayimbidwe.
Bambo Makina atsindika zakufunika koti anthu a ndende akhulupilire Mulungu, ponena kuti mavuto omwe anthuwa akukumana nawo tsiku lina adzatha.
Iwo ati nthawi zina Mulungu amalola dala kuti munthu akumane ndi zowawa ndi cholinga choti pamapeto pake pawoneke ukulu wa Mulungu.
“Ndikuwapempha onse omwe ali mu ndende kuti asamataye mtima, ndipo adzitha kudalira Mulungu nthawi zonse.”
Mau ake wapampando wakwayayi, Innocent Chikhutu anayamikira akhristu a pa parishi yathu ino ya Maula chifukwa chowalandira bwino.
Chikhutu ati akamayenda zimawathandiza chifukwa zimapititsa patsogolo luso lawo.
Wolemba ndi Edwin Sitima









