Akhristu a mphakati wa St. Jude pansi pa parishi ya Our Lady of Africa – Maula Cathedral alimbikitsidwa kukhala okonda kuwerenga Baibulo nthawi zonse.
Pemphori laperekedwa dzulo pa 16 September 2026, ndi Bambo Peter Makina pa maphuziro a Baibulo ku mphakatiwu.




Bambo Makina alimbikitsa akhristuwa kuti akhale ndi chizolowezi chowerenga Baibulo.
“Baibulo ndimmene timadziwa zonse za kulengedwa kwa dziko, kubadwa kwa ambuye Yesu komanso kuwuka kwake, komaso timapeza chikhululupiro chathu Ife aKatolika.”
Pa maphuzirowa, Bambo Makina anapezeraponso mwayi okumbutsa ndi kulimbikitsa akhristu kupita ku tchalitchi nthawi yabwino koma kusathawira pomwe mwambo wansembe ya Misa uli mkati.

