7 October chaka ndi chaka, ana okwana 1 million pa dziko lonse la pansi amatenga nawo gawo pa mapemphero a Kolona.
Ana a Tilitonse komanso Sunday school ochokera ku Maula Cathedral apemphera nawo mapempherowa.
Mapemphero akolona ya anawa anachitika ndi cholinga chakupempherera mtendere komanso umodzi padziko lonse lapansi ndipo anachitikira pa mutu wakuti "Ana khalani amodzi mwa Yesu Khristu, Ogwirizana mu Utumiki."
Izi ndi zithuzi zomwe zikuonetsa anawa akupemphera kolona.













