KUTSEKERA MWEZI WA KOLONA KU PARISHI YA MAULA

Akhristu a pa Parishi ya Our Lady Of Africa – Maula cathedral alimbikitsidwa kukhala okonda kupemphera Kolona.

Bambo mfumu a parishiyi, Bambo Francis Lekaleka ndi amene apereka uthengawu pa mwambo wa nsembe ya Ukaristia yotsekera mwezi wa October, omwe ndi mwezi wopemphera Kolona.

Bambo Lekaleka alimbikitsa akhristu kuti apitirize kupemphera mapempherowa tsiku ndi tsiku kuyambira ku nyumba kwawo, ku miphakati komanso akasonkhana m’magulu ndi m’mabungwe a mumpingo.

Bambo Lekaleka omwenso ndi mkulu wa nthambi yoona za utumiki mu Arkidayosizi ya Lilongwe, ati kudzera m’mapemphero a Kolona, akhristu amapeza zosowa zawo zochuluka, choncho atsindika kufunika kopemphera Kolona tsiku ndi tsiku.

Wolemba ndi Edwin Sitima
Wojambula zithuzi ndi Jerry Matthews Banda

Share the Post:

Related Posts